Luka 16:23 - Buku Lopatulika Ndipo m'dziko la akufa anakweza maso ake, pokhala nao mazunzo, naona Abrahamu patali, ndi Lazaro m'chifuwa mwake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'dziko la akufa anakweza maso ake, pokhala nao mazunzo, naona Abrahamu patali, ndi Lazaro m'chifuwa mwake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene ankazunzika ku Malo a anthu akufa, wachuma uja adayang'ana kumwamba naona Abrahamu ali patali, ndi Lazaro ali pambali pakepa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ali mʼgehena kuzunzika, anakweza maso ake ndipo anaona Abrahamu ali ndi Lazaro pambali pake. |
Pakuti chifundo chanu cha pa ine nchachikulu; ndipo munalanditsa moyo wanga kunsi kwa manda.
Kunsi kwa manda kugwedezeka, chifukwa cha iwe, kukuchingamira podza pako; kukuutsira iwe mizimu, ngakhale onse akuluakulu a dziko lapansi; kukweza kuchokera m'mipando yao mafumu onse a amitundu.
Ndipo iwe, Kapernao, udzakwezedwa kodi kufikira kuthambo? Udzatsika kufikira ku dziko la akufa! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa iwe zikadachitidwa mu Sodomu, uyo ukadakhala kufikira lero.
Ndipo ngati diso lako likukhumudwitsa, ulikolowole, nulitaye: nkwabwino kuti ulowe m'moyo ndi diso limodzi koposa kuponyedwa mu Gehena wamoto, uli ndi maso awiri.
koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.
Koma ngati diso lako lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe, kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losaponyedwa thupi lako lonse mu Gehena.
Ndipo onani, anafuula nati, Tili nanu chiyani, Inu Mwana wa Mulungu? Mwadza kuno kodi kutizunza ife, nthawi yake siinafike?
Ndipo anakweza mau nati, Atate Abrahamu, mundichitire chifundo, mutume Lazaro, kuti aviike nsonga ya chala chake m'madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m'lawi ili la moto.
pakuti ndili nao abale asanu; awachitire umboni iwo kuti iwonso angadze kumalo ano a mazunzo.
Ndipo pakuona Yesu, iye anafuula, nagwa pansi pamaso pake, nati ndi mau aakulu, Ndili nacho chiyani ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikupemphani Inu musandizunze.
Pakuti ngati Mulungu sanalekerere angelo adachimwawo, koma anawaponya kundende nawaika kumaenje a mdima, asungike akaweruzidwe;
Ndipo mdierekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m'nyanja ya moto ndi sulufure, kumeneko kulinso chilombocho ndi mneneri wonyengayo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku kunthawi za nthawi.