Ndipo Ine ndinena kwa inu, Amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo, nadzakwatira wina, achita chigololo: ndipo iye amene akwatira wochotsedwayo, achita chigololo.
Luka 16:18 - Buku Lopatulika Yense wakusudzula mkazi wake, nakwatira wina, achita chigololo; ndipo iye amene akwatira wosudzulidwayo, achita chigololo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yense wakusudzula mkazi wake, nakwatira wina, achita chigololo; ndipo iye amene akwatira wosudzulidwayo, achita chigololo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Aliyense amene asudzula mkazi wake, nakwatira wina, akuchita chigololo. Ndipo amene akwatira mkazi wosudzulidwayo, nayenso akuchita chigololo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Aliyense amene asiya mkazi wake ndi kukakwatira mkazi wina akuchita chigololo, ndipo mwamuna amene akwatira mkazi wosiyidwayo akuchitanso chigololo.” |
Ndipo Ine ndinena kwa inu, Amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo, nadzakwatira wina, achita chigololo: ndipo iye amene akwatira wochotsedwayo, achita chigololo.
Ndipo panali munthu mwini chuma amavala chibakuwa ndi nsalu yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse;
Mkazi alibe ulamuliro wa pa thupi lake la iye yekha, koma mwamuna ndiye; koma momwemonso mwamuna alibe ulamuliro wa pa thupi la iye yekha, koma mkazi ndiye.