Ndipo anansi ake ndi abale ake anamva kuti Ambuye anakulitsa chifundo chake pa iye; nakondwera naye pamodzi.
Luka 15:9 - Buku Lopatulika Ndipo m'mene aipeza amema abwenzi ake ndi anansi ake, nanena, Kondwerani ndi ine, chifukwa ndinapeza ndalama ndidatayayo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'mene aipeza amema abwenzi ake ndi anansi ake, nanena, Kondwerani ndi ine, chifukwa ndinapeza ndalama ndidatayayo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atakapeza amasonkhanitsa abwenzi ake ndi anzake oyandikana nawo, naŵauza kuti, ‘Mukondwere nane pamodzi, chifukwa ndakapeza kandalama kanga kaja kadaatayikaka.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo pamene wayipeza, amayitana anzake, ndi anansi pamodzi nati, ‘Kondwerani nane; ine ndayipeza ndalama yanga yotayika ija.’ |
Ndipo anansi ake ndi abale ake anamva kuti Ambuye anakulitsa chifundo chake pa iye; nakondwera naye pamodzi.
Chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.
Kapena mkazi wanji ali nazo ndalama zasiliva khumi, ngati itayika imodzi, sayatsa nyali, nasesa m'nyumba yake, nafunafuna chisamalire kufikira akaipeza?