kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova, kwa anthu a dziko lapansi pano amene cholowa chao chili m'moyo uno, ndipo mimba yao muidzaza ndi chuma chanu chobisika; akhuta mtima ndi ana, nasiyira ana amakanda zochuluka zao.
Luka 15:12 - Buku Lopatulika ndipo wamng'onoyo anati kwa atate wake, Atate, ndigawirenitu zanga za pa chuma chanu. Ndipo iye anawagawira za moyo wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo wamng'onoyo anati kwa atate wake, Atate, ndigawirenitu zanga za pa chuma chanu. Ndipo iye anawagawira za moyo wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Wamng'ono adapempha bambo wake kuti, ‘Atate, bwanji mugaŵiretu tsopano chuma chanu, ine mundipatsiretu chigawo changa.’ Bamboyo adaŵagaŵiradi ana ake aja chuma chake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wamngʼonoyo anati kwa abambo ake, ‘Abambo, patseni gawo langa la chuma chanu.’ Ndipo iye anawagawira awiriwo chuma chawo. |
kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova, kwa anthu a dziko lapansi pano amene cholowa chao chili m'moyo uno, ndipo mimba yao muidzaza ndi chuma chanu chobisika; akhuta mtima ndi ana, nasiyira ana amakanda zochuluka zao.
pakuti anaponyamo onse mwa zochuluka zao; koma iye anaponya mwa kusowa kwake zonse anali nazo, inde moyo wake wonse.
Ndipo pakupita masiku owerengeka mwana wamng'onoyo anasonkhanitsa zonse, napita ulendo wake kudziko lakutali; ndipo komweko anamwaza chuma chake ndi makhalidwe a chitayiko.
Koma pamene anadza mwana wanu uyu, wakutha zamoyo zanu ndi akazi achiwerewere, munamphera iye mwanawang'ombe wonenepa.