Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Luka 14:7 - Buku Lopatulika

Ndipo Iye ananena fanizo kwa oitanidwa, popenya kuti amadzisankhira mipando yaulemu, nanena kwa iwo,

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Iye ananena fanizo kwa oitanidwa, popenya kuti amadzisankhira mipando yaulemu, nanena kwa iwo,

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yesu adaaona kuti anthu amene adaaitanidwa kudzadya nao ankadzisankhira malo aulemu. Tsono adaŵaphera fanizo, adati,

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iye ataona momwe alendo amasankhira malo aulemu pa tebulo, Iye anawawuza fanizo ili:

Onani mutuwo



Luka 14:7
12 Mawu Ofanana  

Pakuti kunena kwa iwe, Takwera kuno, kupambana ndi kuti utsitsidwe pamaso pa kalonga, amene maso ako anamuona.


Kodi nzeru siitana, luntha ndi kukweza mau ake?


Wobadwa ndi munthu iwe, ipha mwambi, nunene fanizo kwa nyumba ya Israele,


Zonsezi Yesu anaziphiphiritsira m'mafanizo kwa makamu a anthu; ndipo kopanda fanizo sanalankhule kanthu kwa iwo;


nakonda malo a ulemu pamaphwando, ndi mipando ya ulemu m'masunagoge,


Tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mukonda mipando yaulemu m'masunagoge, ndi kupatsidwa moni m'misika.


Chenjerani nao alembi, amene afuna kuyendayenda ovala miinjiro, nakonda kupatsidwa moni m'misika, ndi mipando yaulemu m'sunagoge, ndi malo aulemu pamaphwando;


musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini;


Ndalemba kanthu kwa Mpingo; komatu Diotrefe uja, wofuna kukhala wamkulu wa iwo, satilandira ife.


Nanena nao Samisoni, Mundilole ndikuphereni mwambi; mukanditanthauziratu uwu m'masiku asanuwa a madyerero, ndi kumasulira uwu, ndidzakupatsani malaya a nsalu yabafuta makumi atatu ndi zovala zosinthanitsa makumi atatu;