Luka 14:4 - Buku Lopatulika Koma iwo anakhala chete. Ndipo anamtenga namchiritsa, namuuza apite. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma iwo anakhala chete. Ndipo anamtenga namchiritsa, namuuza apite. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma iwo adangoti chete. Tsono Yesu adatenga munthuyo, ndipo atamchiritsa, adamuuza kuti azipita. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma iwo sanayankhe. Tsono atamutenga munthuyo, Iye anamuchiritsa ndipo anamuwuza kuti azipita. |
Ndipo Yesu anayankha nati kwa achilamulo ndi Afarisi, nanena, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchiritsa, kapena iai?
Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu bulu wake kapena ng'ombe yake itagwa m'chitsime, ndipo sadzaitulutsa pomwepo tsiku la Sabata kodi?