ndipo onani, munali munthu wa dzanja lopuwala. Ndipo anamfunsitsa Iye, ndi kuti, Nkuloleka kodi kuchiritsa tsiku la Sabata? Kuti ampalamulitse mlandu.
Luka 14:3 - Buku Lopatulika Ndipo Yesu anayankha nati kwa achilamulo ndi Afarisi, nanena, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchiritsa, kapena iai? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yesu anayankha nati kwa achilamulo ndi Afarisi, nanena, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchiritsa, kapena iai? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adafunsa akatswiri a Malamulo ndi Afarisi kuti, “Kodi Malamulo amalola kuchiritsa munthu pa tsiku la Sabata, kapena ai?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anafunsa Afarisi ndi akatswiri amalamulo kuti, “Kodi ndi zololedwa kuchiritsa pa tsiku la Sabata kapena ayi?” |
ndipo onani, munali munthu wa dzanja lopuwala. Ndipo anamfunsitsa Iye, ndi kuti, Nkuloleka kodi kuchiritsa tsiku la Sabata? Kuti ampalamulitse mlandu.
Koma Afarisi, pakuona, anati kwa Iye, Tapenyani, ophunzira anu achita chosaloleka tsiku la Sabata.
Ndipo ananena kwa iwo, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchita zabwino, kapena zoipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha? Koma anakhala chete.
Ndipo Iye ananyamuka, naimirira. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ndikufunsani inu, Kodi nkulola tsiku la Sabata, kuchita zabwino, kapena kuchita zoipa? Kupulumutsa moyo, kapena kuuononga?
Ngati munthu alandira mdulidwe tsiku la Sabata, kuti chilamulo cha Mose chingapasulidwe; kodi mundikwiyira Ine, chifukwa ndamchiritsadi munthu tsiku la Sabata?