Luka 14:22 - Buku Lopatulika Ndipo kapoloyo anati, Ambuye, chimene munachilamulira chachitika, ndipo malo atsalapo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kapoloyo anati, Ambuye, chimene munachilamulira chachitika, ndipo malo atsalapo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atabwerako wantchito uja adati, ‘Bwana, ndachita zija munandilamulazi, koma malo akalipobe.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Wantchitoyo anati, ‘Bwana, zimene munanena zachitika koma malo akanalipobe.’ |
Israele, uyembekezere Yehova; chifukwa kwa Yehova kuli chifundo, kwaonso kuchulukira chiombolo.
Ndipo kapoloyo pakubwera anauza mbuye wake zinthu izi. Pamenepo mwini nyumba anakwiya, nati kwa kapolo wake, Tuluka msanga, pita kumakwalala ndi kunjira za mzinda, nubwere nao muno aumphawi ndi opunduka ndi akhungu ndi otsimphina.
Ndipo mbuye ananena kwa kapoloyo, Tuluka, nupite kumiseu ndi njira za kuminda, nuwaumirize anthu alowe, kuti nyumba yanga idzale.
M'nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo.
Kwa ine wochepa ndi wochepetsa wa onse oyera mtima anandipatsa chisomo ichi ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Khristu;
ndipo Iye ndiye chiombolo cha machimo athu; koma wosati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.