Luka 14:10 - Buku Lopatulika Koma pamene paliponse waitanidwa iwe, pita nukhale pansi pa malo a kuthungo; kotero kuti pamene akadza iye anakuitana iwe, akanena ndi iwe, Bwenzi langa, sendera, kwera kuno; pomwepo udzakhala ndi ulemerero pamaso pa onse akuseama pachakudya pamodzi ndi iwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma pamene paliponse waitanidwa iwe, pita nukhale pansi pa malo a kuthungo; kotero kuti pamene akadza iye anakuitana iwe, akanena ndi iwe, Bwenzi langa, sendera, kwera kuno; pomwepo udzakhala ndi ulemerero pamaso pa onse akuseama pachakudya pamodzi ndi iwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma akakuitana, kakhale pa malo otsika, kuti amene adakuitana uja adzakuuze kuti, ‘Bwenzi langa, dzakhale pa malo aulemu pano.’ Apo udzalandira ulemu pamaso pa onse amene uli nao podyera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma akakuyitanani, khalani pa malo otsika, kuti amene anakuyitanani uja adzakuwuzeni kuti, ‘Bwenzi, bwera udzakhale pa malo aulemu pano.’ Pamenepo inu mudzalandira ulemu pamaso pa alendo anzanu onse. |
Ndipo ana aamuna a iwo amene anavuta iwe adzafika, nadzakugwadira; ndipo iwo onse amene anakuchepetsa iwe adzagwadira kumapazi ako, nadzakutcha iwe, Mzinda wa Yehova, Ziyoni wa Woyera wa Israele.
Taona, ndikupatsa ena otuluka m'sunagoge wa Satana akudzinenera okha ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; taona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda.
Nati Samuele, M'mene munali wamng'ono m'maso a inu nokha, kodi simunaikidwe mutu wa mafuko a Israele? Ndipo Yehova anakudzozani mfumu ya Israele.