Mutigwirire ankhandwe, ngakhale aang'ono, amene akuononga minda yamipesa; pakuti m'minda yathu yamipesa muphuka biriwiri.
Luka 13:32 - Buku Lopatulika Ndipo Iye anati kwa iwo, Pitani kauzeni nkhandweyo, Taonani, nditulutsa ziwanda, nditsiriza machiritso lero ndi mawa, ndipo mkucha nditsirizidwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye anati kwa iwo, Pitani kauzeni nkhandweyo, Taonani, nditulutsa ziwanda, nditsiriza machiritso lero ndi mawa, ndipo mkucha nditsirizidwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adati, “Pitani kaiwuzeni nkhandweyo kuti ndikutulutsa mizimu yoipa ndiponso ndikuchiritsa anthu lero ndi maŵa, ndipo mkucha mpamene nditsirize ntchito yanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anayankha kuti, “Pitani kawuzeni nkhandweyo, Ine ndikutulutsa ziwanda ndi kuchiritsa anthu lero ndi mawa ndipo tsiku lachitatu ndidzakwaniritsa cholinga changa.” |
Mutigwirire ankhandwe, ngakhale aang'ono, amene akuononga minda yamipesa; pakuti m'minda yathu yamipesa muphuka biriwiri.
Akalonga ake m'kati mwake ndiwo mikango yobangula; oweruza ake ndi mimbulu ya madzulo, sasiya kanthu ka mawa.
Ndipo mfumu Herode anamva izi; pakuti dzina lake lidamveka; ndipo ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo chifukwa chake mphamvu izi zichitachita mwa Iye.
Yesu anayankha iwo, Ndakuonetsani inu ntchito zabwino zambiri za kwa Atate; chifukwa cha ntchito yiti ya izo mundiponya miyala?
Pamene Yesu tsono adalandira vinyo wosasayo anati, Kwatha; ndipo anawerama mutu, napereka mzimu.
Pakuti kunamuyenera Iye amene zonse zili chifukwa cha Iye, ndi zonse mwa Iye, pakutenga ana ambiri alowe ulemerero, kumkonza wamphumphu mtsogoleri woyamba wa chipulumutso chao mwa zowawa.
ndipo pamene anakonzeka wamphumphu anakhala kwa onse akumvera Iye chifukwa cha chipulumutso chosatha;
Pakuti chilamulo chimaika akulu a ansembe anthu, okhala nacho chifooko; koma mau a lumbirolo, amene anafika chitapita chilamulo, aika Mwana, woyesedwa wopanda chilema kunthawi zonse.