Koma iwo andifuna Ine tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera kudziwa njira zanga; monga mtundu wa anthu ochita chilungamo, osasiya chilangizo cha Mulungu wao, iwo andipempha Ine zilangizo zolungama, nakondwerera kuyandikira kwa Mulungu.
Luka 13:26 - Buku Lopatulika pomwepo mudzayamba kunena, Ife tinadya ndi kumwa pamaso panu, ndipo munaphunzitsa m'makwalala a kwathu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pomwepo mudzayamba kunena, Ife tinadya ndi kumwa pamaso panu, ndipo munaphunzitsa m'makwalala a kwathu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo inuyo mudzayamba kunena kuti, ‘Pajatu tinkadya ndi kumamwa nanu pamodzi, ndipo Inuyo munkaphunzitsa m'miseu ya m'mizinda mwathu.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ndipo inu mudzati, tinkadya ndi kumwa ndi inu ndipo munkaphunzitsa mʼmisewu yathu. |
Koma iwo andifuna Ine tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera kudziwa njira zanga; monga mtundu wa anthu ochita chilungamo, osasiya chilangizo cha Mulungu wao, iwo andipempha Ine zilangizo zolungama, nakondwerera kuyandikira kwa Mulungu.
ndipo Iye adzati, Ndinena kwa inu, sindidziwa kumene muchokera inu; chokani pa Ine, nonse akuchita chosalungama.
Chifukwa chake balani zipatso zakuyenera kulapa mtima, ndipo musayambe kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye ndiye Abrahamu: pakuti ndinena kwa inu, kuti ali ndi mphamvu Mulungu, mwa miyala iyi, kuukitsira Abrahamu ana.
akukhala nao maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.
Avomereza kuti adziwa Mulungu, koma ndi ntchito zao amkana Iye, popeza ali onyansitsa, ndi osamvera, ndi pa ntchito zonse zabwino osatsimikizidwa.