Ndipo ophunzira, pamene anamva, anazizwa kwambiri, nanena, Ngati nkutero angapulumuke ndani?
Luka 13:23 - Buku Lopatulika Ndipo munthu anati kwa Iye, Ambuye, akupulumutsidwa ndiwo owerengeka kodi? Koma Iye anati kwa iwo, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo munthu anati kwa Iye, Ambuye, akupulumutsidwa ndiwo owerengeka kodi? Koma Iye anati kwa iwo, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Munthu wina adamufunsa kuti, “Ambuye, kodi adzapulumuka ndi anthu oŵerengeka okha?” Yesu adayankha kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wina anamufunsa Iye kuti, “Ambuye, kodi ndi anthu ochepa okha amene adzapulumutsidwe?” Iye anawawuza kuti, |
Ndipo ophunzira, pamene anamva, anazizwa kwambiri, nanena, Ngati nkutero angapulumuke ndani?
Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka.
Ndipo Iye anapita pakati pa mizinda ndi midzi, naphunzitsa, nayenda ulendo kunkabe ku Yerusalemu.
Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza; chifukwa anthu ambiri, ndikuuzani, adzafunafuna kulowamo, koma sadzakhoza.