Ndipo Yesu anayendayenda m'mizinda yonse ndi m'midzi, namaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumuwo, nachiritsa nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.
Luka 13:22 - Buku Lopatulika Ndipo Iye anapita pakati pa mizinda ndi midzi, naphunzitsa, nayenda ulendo kunkabe ku Yerusalemu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye anapita pakati pa mizinda ndi midzi, naphunzitsa, nayenda ulendo kunkabe ku Yerusalemu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa ulendo wake wopita ku Yerusalemu, Yesu ankayendera mizinda ndi midzi akuphunzitsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yesu anayendayenda mʼmizinda ndi mʼmidzi, kumaphunzitsa pamene Iye ankapita ku Yerusalemu. |
Ndipo Yesu anayendayenda m'mizinda yonse ndi m'midzi, namaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumuwo, nachiritsa nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.
Ndipo anazizwa chifukwa cha kusakhulupirira kwao. Ndipo anayendayenda m'midzi yozungulirapo, naphunzitsa.
Ndipo munthu anati kwa Iye, Ambuye, akupulumutsidwa ndiwo owerengeka kodi? Koma Iye anati kwa iwo,
Ndipo panali, pamene anayamba kukwanira masiku akuti alandiridwe Iye kumwamba, Yesu anatsimikiza kuloza nkhope yake kunka ku Yerusalemu,
za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.