Koma ndidzafanizira ndi chiyani obadwa awa a makono? Ali ofanana ndi ana akukhala m'mabwalo a malonda, amene alikuitana anzao.
Luka 13:20 - Buku Lopatulika Ndiponso anati, Ndidzafanizira Ufumu wa Mulungu ndi chiyani? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndiponso anati, Ndidzafanizira Ufumu wa Mulungu ndi chiyani? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adatinso, “Ndingayerekezenso ndi chiyani Ufumu wa Mulungu? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anafunsanso kuti, “Kodi ufumu wa Mulungu ndingawufanizire ndi chiyani? |
Koma ndidzafanizira ndi chiyani obadwa awa a makono? Ali ofanana ndi ana akukhala m'mabwalo a malonda, amene alikuitana anzao.
Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, amene anafesa mbeu zabwino m'munda mwake;
Pamenepo ananena, Ufumu wa Mulungu ufanana ndi chiyani? Ndipo ndidzaufanizira ndi chiyani?
Ufanana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi anatenga, nachibisa mu miyeso itatu ya ufa, kufikira unatupo wonsewo.