Ndikuchitire umboni wotani? Ndikuyerekeze ndi chiyani, mwana wamkazi wa Yerusalemu? Ndikulinganize ndi chiyani kuti ndikutonthoze, namwaliwe, mwana wamkazi wa Ziyoni? Popeza akula ngati nyanja; ndani angakuchize?
Luka 13:18 - Buku Lopatulika Pamenepo ananena, Ufumu wa Mulungu ufanana ndi chiyani? Ndipo ndidzaufanizira ndi chiyani? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo ananena, Ufumu wa Mulungu ufanana ndi chiyani? Ndipo ndidzaufanizira ndi chiyani? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adati, “Kodi Ufumu wa Mulungu uli ngati chiyani, ndipo ndingauyerekeze ndi chiyani? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Yesu anafunsa kuti, “Kodi ufumu wa Mulungu uli ngati chiyani? Kodi Ine ndingawufanizire ndi chiyani? |
Ndikuchitire umboni wotani? Ndikuyerekeze ndi chiyani, mwana wamkazi wa Yerusalemu? Ndikulinganize ndi chiyani kuti ndikutonthoze, namwaliwe, mwana wamkazi wa Ziyoni? Popeza akula ngati nyanja; ndani angakuchize?
Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, amene anafesa mbeu zabwino m'munda mwake;
ndipo sadzanena, Taonani uwu, kapena uwo! Pakuti, taonani, Ufumu wa Mulungu uli m'kati mwa inu.