Luka 13:17 - Buku Lopatulika Ndipo pamene Iye anatero, onse aja akutsutsana naye ananyazitsidwa; ndipo anthu onse a m'khamu anakondwera ndi zinthu zonse za ulemererozo zinachitidwa ndi Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene Iye anatero, onse aja akutsutsana naye ananyazitsidwa; ndipo anthu onse a m'khamu anakondwera ndi zinthu zonse za ulemererozo zinachitidwa ndi Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu atanena zimenezi, adani ake onse adachita manyazi. Koma anthu ena onse adakondwera chifukwa cha ntchito zodabwitsa zimene Iye ankachita. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atanena izi, onse omutsutsa anachititsidwa manyazi, koma anthu anakondwera ndi zodabwitsa zonse zimene Iye anazichita. |
Achite manyazi nadodome iwo akulondola moyo wanga kuti auononge. Abwerere m'mbuyo, nachite manyazi iwo okondwera kundichitira choipa.
Afanana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera, woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa?
Tsiku limenelo mphukira ya Yehova idzakhala yokongola ndi ya ulemerero, chipatso cha nthaka chidzakhala chokometsetsa ndi chokongola, kwa iwo amene adzapulumuka a Israele.
Koma mwa Yehova yekha, wina adzati kwa Ine, muli chilungamo ndi mphamvu; ngakhale kwa Iyeyo anthu adzafika, ndi onse amene anamkwiyira, adzakhala ndi manyazi.
Imvani mau a Yehova, inu amene munthunthumira ndi mau ake; abale anu amene akudani inu, amene anaponya inu kunja chifukwa cha dzina langa, iwo anati, Yehova alemekezedwe, kuti ife tione kusangalala kwanu; koma iwo adzakhala ndi manyazi.
Ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata Iye, ndi kulemekeza Mulungu: ndipo anthu onse pakuona, anachitira Mulungu mayamiko.
Koma m'mene anawaopsanso anawamasula, osapeza kanthu kakuwalanga, chifukwa cha anthu; pakuti onse analemekeza Mulungu chifukwa cha chomwe chidachitika.
Koma sadzapitirirapo; pakuti kupusa kwao kudzaonekeratu kwa onse, monganso kupusa kwa iwo aja.
mau olama osatsutsika; kuti iye wakutsutsana achite manyazi, posakhala nako kanthu koipa kakutinenera ife.
ndi kukhala nacho chikumbumtima chabwino, kuti umo akunenerani, iwo akunenera konama mayendedwe anu abwino mu Khristu akachitidwe manyazi.