Natuluka Satana pamaso pa Yehova, nazunza Yobu ndi zilonda zowawa, kuyambira kuphazi lake kufikira pakati pamutu pake.
Luka 13:11 - Buku Lopatulika Ndipo mkazi anali nao mzimu wakumdwalitsa zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu; nakhala wopeteka, ndimo analibe mphamvu konse yakuweramuka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mkazi anali nao mzimu wakumdwalitsa zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu; nakhala wopeteka, ndimo analibe mphamvu konse yakuweramuka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa M'menemo munali mai wina amene anali ndi mzimu woipa umene udamudwalitsa zaka 18. Anali ndi msana wokhota, mwakuti sankatha konse kuŵeramuka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo momwemo munali mayi amene anali ndi mzimu woyipa umene unamudwalitsa zaka 18. Iye anali wokhota msana ndipo samatha kuweramuka ndi pangʼono pomwe. |
Natuluka Satana pamaso pa Yehova, nazunza Yobu ndi zilonda zowawa, kuyambira kuphazi lake kufikira pakati pamutu pake.
Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikanso chifukwa cha chipulumutso cha nkhope yake.
Mundichitire chifundo, Yehova; pakuti ndalefuka ine. Mundichize, Yehova; pakuti anthunthumira mafupa anga.
Ndipo Yesu anayendayenda mu Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.
Ndipo Iye anafunsa atate wake, kuti, Chimenechi chinayamba kumgwira liti? Ndipo anati, Chidamyamba akali mwana.
Ndipo Yesu m'mene anamuona, anamuitana, nanena naye, Mkaziwe, wamasulidwa kudwala kwako.
Ndipo mkazi uyu, ndiye mwana wa Abrahamu, amene Satana anammanga, onani, zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu, nanga si kuyenera kodi, kuti amasulidwe nsinga yake imeneyi tsiku la Sabata?
Koma poyamba kuchitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiomboledwe chanu chayandikira.
ndi akazi ena amene anachiritsidwa ziwanda ndi nthenda zao, ndiwo, Maria wonenedwa Magadala, amene ziwanda zisanu ndi ziwiri zinatuluka mwa iye,
Ndipo atatuluka pamtunda Iye, anakomana naye mwamuna wa kumzinda, amene anali nazo ziwanda; ndipo masiku ambiri sanavale chovala, nisanakhala m'nyumba, koma m'manda.
Ndipo mkazi, anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, amene adasudzula asing'anga za moyo wake zonse, ndipo sanathe kuchiritsidwa ndi mmodzi yense,
Ndipo munthu wina wopunduka miyendo chibadwire ananyamulidwa, amene akamuika masiku onse pa khomo la Kachisi lotchedwa Lokongola, kuti apemphe zaulere kwa iwo akulowa mu Kachisi;
Pakuti anali wa zaka zake zoposa makumi anai munthuyo, amene chizindikiro ichi chakumchiritsa chidachitidwa kwa iye.