Onani Yehova, nimupenye, mwachitira ayani ichi? Kodi akazi adzadya zipatso zao, kunena ana amene anawalera wokha? Kodi wansembe ndi mneneri adzaphedwa m'malo opatulika a Ambuye?
Luka 13:1 - Buku Lopatulika Ndipo anakhalako nthawi yomweyo, anthu ena amene anamuuza Iye za Agalileya, amene Pilato anasakaniza mwazi wao ndi nsembe zao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anakhalako nthawi yomweyo, anthu ena amene anamuuza Iye za Agalileya, amene Pilato anasanganiza mwazi wao ndi nsembe zao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu ena amene anali pomwepo adadza kwa Yesu, nayamba kumsimbira za Agalileya amene Pilato adaalamula kuti aphedwe, pamene iwo ankapereka nsembe zao kwa Mulungu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi yomweyo panali ena amene analipo omwe amamuwuza Yesu za Agalileya amene magazi awo Pilato anawasakaniza ndi nsembe zawo. |
Onani Yehova, nimupenye, mwachitira ayani ichi? Kodi akazi adzadya zipatso zao, kunena ana amene anawalera wokha? Kodi wansembe ndi mneneri adzaphedwa m'malo opatulika a Ambuye?
Ndipo pakudza mamawa, ansembe aakulu ndi akulu a anthu onse anakhala upo wakumchitira Yesu, kuti amuphe;
amenenso anati, Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang'ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kunka Kumwamba kuchokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba.
Ndipo anadabwa onse, nazizwa, nanena, Taonani, awa onse alankhulawa sali Agalileya kodi?
Atapita ameneyo, anauka Yudasi wa ku Galileya, masiku a kalembera, nakopa anthu amtsate. Iyeyunso anaonongeka, ndi onse amene anamvera iye anabalalitsidwa.