Luka 12:44 - Buku Lopatulika Ndinena ndinu zoona, kuti adzamuika iye kapitao wa pa zonse ali nazo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinena ndinu zoona, kuti adzamuika iye kapitao wa pa zonse ali nazo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndithu ndikunenetsa kuti adzamuika woyang'anira chuma chake chonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti adzamuyika kukhala woyangʼanira katundu wake yense. |
Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako.
Koma kapolo uyo akanena mumtima mwake, Mbuye wanga azengereza kudza; ndimo akayamba kupanda anyamata ndi adzakazi ndi kudya ndi kumwa, ndi kuledzera;
ndikulangiza ugule kwa Ine golide woyengeka m'moto, kuti ukakhale wachuma, ndi zovala zoyera, kuti ukadziveke, ndi kuti manyazi a usiwa wako asaoneke; ndi mankhwala opaka m'maso mwako, kuti ukaone.