Luka 12:41 - Buku Lopatulika Ndipo Petro anati, Ambuye, kodi fanizo ili mwalinena kwa ife, kapena kwa onse? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Petro anati, Ambuye, kodi fanizo ili mwalinena kwa ife, kapena kwa onse? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Petro adati, “Ambuye, kodi fanizoli mukuphera ife tokha, kapena mukuuza onse?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Petro anafunsa kuti, “Kodi mukunena fanizoli kwa ife, kapena kwa aliyense?” |
Ndipo anadza nawapeza iwo ali m'tulo, nanena ndi Petro, Simoni, ugona kodi? Unalibe mphamvu yakudikira ora limodzi kodi?
Ndipo kapolo uyo, wodziwa chifuniro cha mbuye wake, ndipo sanakonze, ndi kusachita zonga za chifuniro chakecho, adzakwapulidwa mikwapulo yambiri.
Koma iye amene sanachidziwe, ndipo anazichita zoyenera mikwapulo, adzakwapulidwa pang'ono. Ndipo kwa munthu aliyense adampatsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri; ndipo amene anamuikizira zambiri, adzamuuza abwezere zoposa.
Koma chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi; chifukwa chake khalani anzeru, ndipo dikirani m'mapemphero;
Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire: