Ndipo panali pamene anawatulutsa iwo kunja, anati, Tapulumuka ndi moyo wako; usacheuke, usakhale pachigwa paliponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke.
Luka 12:23 - Buku Lopatulika Pakuti moyo uli woposa chakudya, ndi thupi liposa chovala. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti moyo uli woposa chakudya, ndi thupi liposa chovala. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakuti moyo umaposa chakudya, ndipo thupi limaposa zovala. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Moyo uposa chakudya, ndi thupi liposa chovala. |
Ndipo panali pamene anawatulutsa iwo kunja, anati, Tapulumuka ndi moyo wako; usacheuke, usakhale pachigwa paliponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke.
Nati Yehova kwa Satana, Taona, zonse ali nazo zikhale m'dzanja mwako; pa iye pokha usatambasula dzanja lako. Natuluka Satana pamaso pa Yehova.
Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake.
Ndipo Iye anati kwa ophunzira ake, Chifukwa chake ndinena ndinu, Musade nkhawa ndi moyo wanu, chimene mudzadya; kapena ndi thupi lanu, chimene mudzavala.
Lingirirani makwangwala, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri!