Koma Yehova ananena naye, Anampangira munthu m'kamwa ndani? Kapena analenga munthu wosalankhula ndani, kapena wogontha, kapena wamaso, kapena wakhungu? Si ndine Yehova kodi?
Luka 12:12 - Buku Lopatulika pakuti Mzimu Woyera adzaphunzitsa inu nthawi yomweyo zimene muyenera kuzinena. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pakuti Mzimu Woyera adzaphunzitsa inu nthawi yomweyo zimene muyenera kuzinena. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Popeza kuti Mzimu Woyera adzakudziŵitsani pa nthaŵi yomweyo zimene mudzayenera kunena.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero pakuti Mzimu Woyera nthawi imeneyo adzakuphunzitsani zoyenera kunena.” |
Koma Yehova ananena naye, Anampangira munthu m'kamwa ndani? Kapena analenga munthu wosalankhula ndani, kapena wogontha, kapena wamaso, kapena wakhungu? Si ndine Yehova kodi?
Ndipo tsopano muka, ndipo Ine ndidzakhala m'kamwa mwako, ndi kukuphunzitsa chomwe ukalankhule.
Koma pamene paliponse angakuperekeni inu, musamadera nkhawa mudzalankhule bwanji kapena mudzanene chiyani; pakuti chimene mudzachilankhula, chidzapatsidwa kwa inu nthawi yomweyo;
Ndipo munthu wa m'khamulo anati kwa Iye, Mphunzitsi, uzani mbale wanga agawane ndi ine chuma chamasiye.
Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.
Pamenepo Petro, wodzala ndi Mzimu Woyera anati kwa iwo, Oweruza a anthu inu, ndi akulu,
Koma iye, pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, anapenyetsetsa Kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuimirira padzanja lamanja la Mulungu,