Ndipo Yesu ananena, Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziwa chimene achita. Ndipo anagawana zovala zake, poyesa maere.
Luka 12:10 - Buku Lopatulika Ndipo aliyense amene adzanenera Mwana wa Munthu zoipa adzakhululukidwa; koma amene anenera Mzimu Woyera zamwano sadzakhululukidwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo amene aliyense adzanenera Mwana wa Munthu zoipa adzakhululukidwa; koma amene anenera Mzimu Woyera zamwano sadzakhululukidwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Aliyense wonenera zoipa Mwana wa Munthu, Mulungu adzamkhululukira, koma wonyoza Mzimu Woyera ndi mau achipongwe, Mulungu sadzamkhululukira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo aliyense amene ayankhulira Mwana wa Munthu mawu oyipa adzakhululukidwa, koma iye wochitira mwano Mzimu Woyera sadzakhululukidwa. |
Ndipo Yesu ananena, Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziwa chimene achita. Ndipo anagawana zovala zake, poyesa maere.
ndingakhale kale ndinali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wachipongwe; komatu anandichitira chifundo, popeza ndinazichita wosazindikira, wosakhulupirira;
Wina akaona mbale wake alikuchimwa tchimo losati la kuimfa, apemphere Mulungu, ndipo Iye adzampatsira moyo wa iwo akuchita machimo osati a kuimfa. Pali tchimo la kuimfa: za ililo sindinena kuti mupemphere.