Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu adzakhala ndi bwenzi lake, nadzapita kwa iye pakati pa usiku, nadzati kwa iye, Bwenzi, ndibwereke mikate itatu;
Luka 11:6 - Buku Lopatulika popeza wandidzera bwenzi langa lochokera paulendo ndipo ndilibe chompatsa; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 popeza wandidzera ndipo ndilibe chompatsa; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kwafika bwenzi langa, ali pa ulendo, ndipo ndilibe choti ndingampatse.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero chifukwa ndalandira bwenzi langa amene ali pa ulendo ndipo ine ndilibe choti ndimupatse.’ |
Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu adzakhala ndi bwenzi lake, nadzapita kwa iye pakati pa usiku, nadzati kwa iye, Bwenzi, ndibwereke mikate itatu;
ndipo iyeyu wa m'katimo poyankha akati, Usandivuta; pakhomo mpotseka tsopano, ndipo ana anga ali nane pamodzi pogona; sindingathe kuuka ndi kukupatsa?