Ndipo kunali atawerenga kalatayo mfumu ya Israele, anang'amba zovala zake, nati, Ngati ndine Mulungu, kupha ndi kubwezera moyo, kuti ameneyo atumiza kwa ine kumchiritsa munthu khate lake? Pakuti dziwani, nimupenye, kuti alikufuna chifukwa pa ine.
Luka 11:54 - Buku Lopatulika namlindira akakole kanthu kotuluka m'kamwa mwake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 namlindira akakole kanthu kotuluka m'kamwa mwake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Cholinga chao chinali chofuna kumtapa m'kamwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero pofuna kumukola muchina chilichonse chimene Iye angayankhule. |
Ndipo kunali atawerenga kalatayo mfumu ya Israele, anang'amba zovala zake, nati, Ngati ndine Mulungu, kupha ndi kubwezera moyo, kuti ameneyo atumiza kwa ine kumchiritsa munthu khate lake? Pakuti dziwani, nimupenye, kuti alikufuna chifukwa pa ine.
Ndipo anatuma kwa Iye ena a Afarisi ndi a Aherode, kuti akamkole Iye m'kulankhula kwake.
Ndipo pamene Iye anatuluka m'menemo, alembi ndi Afarisi anayamba kumuumiriza Iye kolimba, ndi kumfunsa zinthu zambiri;
Ndipo anamyang'anira, natumiza ozonda, amene anadzionetsera ngati olungama mtima, kuti akamkole pa mau ake, kotero kuti akampereke Iye ku ukulu ndi ulamuliro wa kazembe.
Ndipo sanakhoze kugwira mauwo pamaso pa anthu; ndipo anazizwa ndi kuyankha kwake, nakhala chete.
Pamenepo musakopedwe nao; pakuti amlalira iye oposa makumi anai a iwo amene anadzitemberera okha kuti sadzadya kapena kumwa kufikira atamupha iye; ndipo akonzekeratu tsopano nayang'anira lonjezano lanu.