Aramu patsogolo ndi Afilisti pambuyo; ndipo iwo adzadya Israele ndi kukamwa koyasama. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.
Luka 11:53 - Buku Lopatulika Ndipo pamene Iye anatuluka m'menemo, alembi ndi Afarisi anayamba kumuumiriza Iye kolimba, ndi kumfunsa zinthu zambiri; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene Iye anatuluka m'menemo, alembi ndi Afarisi anayamba kumuumiriza Iye kolimba, ndi kumtompha Iye ndi zinthu zambiri; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene Yesu adatuluka m'nyumbamo, aphunzitsi a Malamulo pamodzi ndi Afarisi adayamba kumzonda ndi kumpanikiza ndi mafunso ambiri ozunguza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene Yesu anachokamo, Afarisi ndi aphunzitsi a Malamulo anayamba kumamutsutsa koopsa ndi kumupanikiza ndi mafunso, |
Aramu patsogolo ndi Afilisti pambuyo; ndipo iwo adzadya Israele ndi kukamwa koyasama. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.
Ndipo iwo anati, Tiyeni, tilingalire Yeremiya chomchitira choipa; pakuti chilamulo sichidzathera wansembe, kapena uphungu wanzeru, kapena mau mneneri. Tiyeni, timpande iye ndi lilime, tisamvere iye mau ake ali onse.
Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzampambana iye, ndipo tidzambwezera chilango.
Tsoka inu, achilamulo! Chifukwa munachotsa chifungulo cha nzeru; inu simunalowamo nokha, ndipo munawaletsa iwo analinkulowa.
Ndipo anamyang'anira, natumiza ozonda, amene anadzionetsera ngati olungama mtima, kuti akamkole pa mau ake, kotero kuti akampereke Iye ku ukulu ndi ulamuliro wa kazembe.
Ndipo anadza kwa Iye Asaduki ena, amene amanena kuti palibe kuuka kwa akufa; ndipo anamfunsa Iye,
Inedi ndinayesa ndekha, kuti kundiyenera kuchita zinthu zambiri zotsutsana nalo dzina la Yesu Mnazarayo.
sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa;
Kotero kuti tinadandaulira Tito, kuti monga anayamba kale, chomwechonso atsirize kwa inu chisomo ichinso.