Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwake, koma adzala m'katimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse.
Luka 11:47 - Buku Lopatulika Tsoka inu! Chifukwa mumanga za pa manda a aneneri, ndipo makolo anu anawapha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsoka inu! Chifukwa mumanga za pa manda a aneneri, ndipo makolo anu anawapha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Muli ndi tsoka, chifukwa mumamanga ziliza za aneneri, pamene ndi makolo anu omwe akale amene adapha aneneriwo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Tsoka kwa inu, chifukwa mumawaka manda a aneneri, komatu ndi makolo anu amene anawapha. |
Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwake, koma adzala m'katimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse.
Chomwecho muli mboni, ndipo muvomera ntchito za makolo anu; chifukwa iwotu anawapha, koma inu muwamangira iwo zapamanda.
Ouma khosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu Woyera nthawi zonse; monga anachita makolo anu, momwemo inu.
amene adaphanso Ambuye Yesu, ndi aneneri, natilondalonda ife, ndipo sakondweretsa Mulungu, natsutsana nao anthu onse;