Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Luka 11:44 - Buku Lopatulika

Tsoka inu! Chifukwa muli ngati manda osaoneka, ndipo anthu akuyendayenda pamwamba pao sadziwa.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Tsoka inu! Chifukwa muli ngati manda osaoneka, ndipo anthu akuyendayenda pamwamba pao sadziwa.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Muli ndi tsoka, chifukwa muli ngati manda osazindikirika, amene anthu amapondapo osadziŵa kanthu.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa muli ngati manda osawaka, amene anthu amangoyendapo, osawadziwa.”

Onani mutuwo



Luka 11:44
7 Mawu Ofanana  

Pakuti m'kamwa mwao mulibe mau okhazikika; m'kati mwao m'mosakaza; m'mero mwao ndi manda apululu; lilime lao asyasyalika nalo.


Ndipo opitapitawo adzapitapita m'dziko, ndipo wina akaona fupa la munthu aikepo chizindikiro, mpaka oikawo aliika m'chigwa cha unyinji wa Gogi.


Efuremu ndiye wozonda kwa Mulungu wanga; kunena za mneneri, msampha wa msodzi uli m'njira zake zonse, ndi udani m'nyumba ya Mulungu wake.


Ndipo aliyense wakukhudza munthu wophedwa ndi lupanga, kapena mtembo, kapena fupa la munthu, kapena manda, pathengo poyera, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.


kamene kakhaladi kakang'ono koposa mbeu zonse, koma katakula, kali kakakulu kuposa zitsamba zonse, nukhala mtengo, kotero kuti mbalame za mlengalenga zimadza, nkubindikira mu nthambi zake.


Pamenepo Paulo anati kwa iye, Mulungu adzakupanda iwe, khoma loyeretsedwa iwe; ndipo kodi ukhala iwe wakundiweruza mlandu monga mwa chilamulo, ndipo ulamulira andipande ine posanga chilamulo?