Luka 11:43 - Buku Lopatulika Tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mukonda mipando yaulemu m'masunagoge, ndi kupatsidwa moni m'misika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mukonda mipando yaulemu m'masunagoge, ndi kupatsidwa moni m'misika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Muli ndi tsoka, inu Afarisi, chifukwa mumakonda mipando yaulemu m'nyumba zamapemphero, ndiponso kuti anthu azikupatsani moni waulemu pa misika. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa mumakonda mipando yofunika kwambiri mʼmasunagoge ndi malonje mʼmalo a pa msika. |
Koma ndidzafanizira ndi chiyani obadwa awa a makono? Ali ofanana ndi ana akukhala m'mabwalo a malonda, amene alikuitana anzao.
Chenjerani nao alembi, amene afuna kuyendayenda ovala miinjiro, nakonda kupatsidwa moni m'misika, ndi mipando yaulemu m'sunagoge, ndi malo aulemu pamaphwando;
M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;
musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini;
Ndalemba kanthu kwa Mpingo; komatu Diotrefe uja, wofuna kukhala wamkulu wa iwo, satilandira ife.