Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pang'ombe, ndi padziko lonse lapansi, ndi pazokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi.
Luka 11:40 - Buku Lopatulika Opusa inu, kodi Iye wopanga kunja kwake sanapangenso m'kati mwake? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Opusa inu, kodi Iye wopanga kunja kwake sanapangenso m'kati mwake? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndinu anthu opusa! Kodi Mulungu amene adapanga zakunja, si yemweyo adapanganso zam'kati? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu opusa inu! Kodi amene anapanga zamʼkati sanapangenso zakunja? |
Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pang'ombe, ndi padziko lonse lapansi, ndi pazokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi.
Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.
Wauchitsiru amati mumtima mwake, Kulibe Mulungu. Achita zovunda, achita ntchito zonyansa; kulibe wakuchita bwino.
Kodi mudzakonda zazibwana kufikira liti, achibwana inu? Onyoza ndi kukonda kunyoza, opusa ndi kuda nzeru?
Tamvanitu ichi, inu anthu opusa, ndi opanda nzeru; ali ndi maso koma osaona, ali ndi makutu koma osamva;
Katundu wa mau a Yehova wakunena Israele. Atero Yehova, wakuyala miyamba, ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kulenga mzimu wa munthu m'kati mwake;
Ndipo anagwa nkhope zao pansi, nati, Mulungu, ndinu Mulungu wa mizimu ya anthu onse, walakwa munthu mmodzi, ndipo kodi mukwiya nalo khamu lonse?
Inu opusa, ndi akhungu: pakuti choposa nchiti, golide kodi, kapena Kachisi amene ayeretsa golideyo?
Mfarisi iwe wakhungu, yambawatsuka m'kati mwa chikho ndi mbale, kuti kunja kwake kukhalenso koyera.
Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani?
Ndipo Iye anati kwa iwo, Opusa inu, ndi ozengereza mtima kusakhulupirira zonse adazilankhula aneneri!
Komanso, tinali nao atate a thupi lathu akutilanga, ndipo tinawalemekeza; kodi sitidzagonjera Atate wa mizimu koposa nanga, ndi kukhala ndi moyo?