Koma iwo akupatula kutsata njira zao zokhotakhota, Yehova adzawachotsa pamodzi ndi ochita zopanda pake. Mtendere ukhale pa Israele.
Luka 11:25 - Buku Lopatulika ndipo pofika, uipeza yosesa ndi yokonzeka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo pofika, uipeza yosesa ndi yokonzeka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ukafika, umapeza m'nyumba muja muli mosesasesa ndi mokonza bwino. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ukafika umapeza mʼnyumba mosesedwa bwino ndi mokonza. |
Koma iwo akupatula kutsata njira zao zokhotakhota, Yehova adzawachotsa pamodzi ndi ochita zopanda pake. Mtendere ukhale pa Israele.
Mau a pakamwa pake ndiwo opanda pake ndi onyenga, waleka kuzindikira ndi kuchita bwino.
Pamene paliponse mzimu wonyansa ukatuluka mwa munthu, upyola malo opanda madzi nufunafuna mpumulo; ndipo posaupeza unena, Ndidzabwera kunyumba kwanga kumene ndinatulukako;
Pomwepo upita nutenga mizimu ina isanu ndi iwiri yoipa yoposa ndi uwu mwini; ndipo ilowa nikhalira komweko; ndipo makhalidwe otsiriza a munthu uyu aipa koposa oyambawo.