Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Luka 11:21 - Buku Lopatulika

Pamene paliponse mwini mphamvu alonda pabwalo pake zinthu zake zili mumtendere;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pamene paliponse mwini mphamvu alonda pabwalo pake zinthu zake zili mumtendere;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

“Munthu wamphamvu akamalonda nyumba yake ali ndi zida zankhondo, katundu wake amakhala pabwino.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Munthu wamphamvu, amene ali ndi zida, akamalondera nyumba yake, katundu wake amatetezedwa.

Onani mutuwo



Luka 11:21
5 Mawu Ofanana  

Kodi chofunkha chingalandidwe kwa wamphamvu, pena am'nsinga a woopsa angapulumutsidwe?


Kapena akhoza bwanji munthu kulowa m'banja la munthu wolimba, ndi kufunkha akatundu ake, ngati iye sayamba kumanga munthu wolimbayo? Ndipo pamenepo adzafunkha za m'banja lake.


Komatu palibe munthu akhoza kulowa m'nyumba ya mwini mphamvu, ndi kufunkha akatundu ake, koma ayambe wamanga mwini mphamvuyo; ndipo pamenepo adzafunkha za m'nyumba mwake.


Koma ngati Ine nditulutsa ziwanda ndi chala cha Mulungu, pamenepo Ufumu wa Mulungu wafikira inu.


koma pamene paliponse amdzera wakumposa mphamvu, nakamgonjetsa, amchotsera zida zake zonse zimene anazitama, nagawa zofunkha zake.