Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba; pakuti m'chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m'dziko loti see.
Luka 11:14 - Buku Lopatulika Ndipo analikutulutsa chiwanda chosalankhula. Ndipo kunali, chitatuluka chiwanda, wosalankhulayo analankhula; ndipo makamu a anthu anazizwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo analikutulutsa chiwanda chosalankhula. Ndipo kunali, chitatuluka chiwanda, wosalankhulayo analankhula; ndipo makamu a anthu anazizwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsiku lina Yesu ankatulutsa mzimu woipa woletsa munthu kulankhula. Mzimuwo utatuluka, munthu amene anali wosalankhulayo adayamba kulankhula, mwakuti anthu ambirimbiri amene anali pomwepo adazizwa kwabasi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu amatulutsa chiwanda chimene chinali chosayankhula. Chiwandacho chitatuluka, munthu wosayankhulayo anayankhula, ndipo gulu la anthu linadabwa. |
Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba; pakuti m'chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m'dziko loti see.
Ndipo pakumva ichi, Yesu anazizwa, nati kwa iwo akumtsata, Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mwa Israele, sindinapeze chikhulupiriro chotere.