Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Luka 11:12 - Buku Lopatulika

Kapena akadzampempha dzira kodi adzampatsa chinkhanira?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Kapena akadzampempha dzira kodi adzampatsa chinkhanira?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kapena atampempha dzira, iye nkumupatsa chinkhanira?

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kapena atapempha dzira, kodi mungamupatse chinkhanira?

Onani mutuwo



Luka 11:12
5 Mawu Ofanana  

Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu iwe, usawaopa, kapena kuopa mau ao; ingakhale mitungwi ndi minga ikhala ndi iwe, nukhala pakati pa zinkhanira, usaopa mau ao kapena kuopsedwa ndi nkhope zao; pakuti ndiwo nyumba yopanduka.


Taonani, ndakupatsani ulamuliro wakuponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi pa mphamvu iliyonse ya mdaniyo; ndipo kulibe kanthu kadzakuipsani konse.


Ndipo ndani wa inu ali atate, mwana wake akadzampempha mkate, adzampatsa mwala? Kapena nsomba, nadzamninkha njoka m'malo mwa nsomba?


Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye?


Ndipo lili nayo michira yofanana ndi ya chinkhanira ndi mbola; ndipo m'michira mwao muli mphamvu yao yakuipsa anthu miyezi isanu.