Ndipo ine, pakutenga nkhawa, ndinati, Ndadulidwa kundichotsa pamaso panu. Komatu munamva mau a kupemba kwanga pamene ndinafuulira kwa Inu.
Luka 11:10 - Buku Lopatulika Pakuti yense wakupempha alandira; ndi wofunayo apeza; ndi iye amene agogoda adzamtsegulira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti yense wakupempha alandira; ndi wofuna apeza; ndi iye amene agogoda adzamtsegulira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja munthu amene amapempha, ndiye amalandira, amene amafunafuna, ndiye amapeza, ndipo amene amagogoda, ndiye amamtsekulira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti aliyense amene amapempha amalandira. Munthu amene amafunafuna amapeza. Iye amene amagogoda amamutsekulira. |
Ndipo ine, pakutenga nkhawa, ndinati, Ndadulidwa kundichotsa pamaso panu. Komatu munamva mau a kupemba kwanga pamene ndinafuulira kwa Inu.
pakuti yense wakupempha alandira; ndi wakufunayo apeza; ndi kwa wogogodayo chitsegulidwa.
Ndipo ndani wa inu ali atate, mwana wake akadzampempha mkate, adzampatsa mwala? Kapena nsomba, nadzamninkha njoka m'malo mwa nsomba?
Ndipo Ine ndinena ndi inu, Pemphani, ndipo adzakupatsani; funani, ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsegulirani.
Mupempha, ndipo simulandira, popeza mupempha koipa, kuti mukachimwaze pochita zikhumbitso zanu.
Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.