Ndipo pamene panali madzulo, ophunzira ake anafika kwa Iye, nanena, Malo ano nga chipululu, ndipo nthawi yapita tsopano; kauzeni makamuwo amuke, apite kumidzi kukadzigulira okha kamba.
Luka 10:40 - Buku Lopatulika Koma Marita anatekeseka ndi kutumikira kwambiri; ndipo anadzako nati, Ambuye, kodi simusamala kuti mbale wanga anandisiya nditumikire ndekha? Mumuuze tsono kuti andithandize. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Marita anatekeseka ndi kutumikira kwambiri; ndipo anadzako nati, Ambuye, kodi simusamala kuti mbale wanga anandisiya nditumikire ndekha? Mumuuze tsono kuti andithandize. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Marita ankatanganidwa ndi ntchito zambiri. Choncho adapita kwa Yesu nati, “Ambuye, kodi simukusamalako kuti mng'ono wangayu akundilekera ndekha ntchito? Muuzeni adzandithandize.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Marita anatanganidwa ndi zokonzekera zonse zimene zimayenera kuchitika. Iye anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Ambuye, kodi simusamala kuti mchemwali wanga wandisiya kuti ndichite ntchito yonse ndekha? Muwuzeni andithandize!” |
Ndipo pamene panali madzulo, ophunzira ake anafika kwa Iye, nanena, Malo ano nga chipululu, ndipo nthawi yapita tsopano; kauzeni makamuwo amuke, apite kumidzi kukadzigulira okha kamba.
Ndipo Petro anamtenga Iye, nayamba kumdzudzula, kuti, Dzichitireni chifundo, Ambuye; sichidzatero kwa Inu ai.
Ndipo pakupita paulendo pao Iye analowa m'mudzi wina; ndipo mkazi wina dzina lake Marita anamlandira Iye kunyumba kwake.
Koma Ambuye anayankha nati kwa iye, Marita, Marita, uda nkhawa nuvutika ndi zinthu zambiri;
Koma panali munthu wodwala, Lazaro wa ku Betaniya, wa m'mudzi wa Maria ndi mbale wake Marita.
Ndipo anamkonzera Iye chakudya komweko; ndipo Marita anatumikira; koma Lazaro anali mmodzi wa iwo akuseama pachakudya pamodzi ndi Iye.
Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitayika koma cha chakudya chimene chitsalira kumoyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro.