Luka 10:32 - Buku Lopatulika Momwemonso Mlevi, pofika pamenepo, ndi kumuona, anapita mbali ina. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Momwemonso Mlevi, pofika pamenepo, ndi kumuona, anapita mbali ina. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chimodzimodzinso Mlevi wina adafika pamalopo, ndipo pamene adaona munthuyo, nayenso adangolambalala. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chimodzimodzinso, Mlevi wina pamene anafika pa malopo ndi kumuona, analambalalanso. |
Mnzako, ndi mnzake wa atate wako, usawasiye; usanke kunyumba ya mbale wako tsiku la tsoka lako; mnansi wapafupi aposa mbale wakutali.
Kodi si ndiko kupatsa chakudya chako kwa anjala, ndi kuti ubwere nao kunyumba kwako aumphawi otayika? Pakuona wamaliseche kuti umveke, ndi kuti usadzibisire wekha a chibale chako?
Ndipo kudangotero kuti wansembe wina anatsika njirayo, ndipo pakumuona iye anapita mbali ina.
Koma Msamariya wina ali pa ulendo wake anadza pali iye; ndipo pakumuona, anagwidwa chifundo,
Ndipo anamgwira Sostene, mkulu wa sunagoge, nampanda kumpando wachiweruziro. Ndipo Galio sanasamalire zimenezi.
Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika,