Luka 10:30 - Buku Lopatulika Ndipo Yesu anamlanda mau, nati, Munthu wina anatsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Yeriko; ndipo anagwa m'manja a achifwamba amene anamvula zovala, namkwapula, nachoka atamsiya wofuna kufa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yesu anamlanda mau, nati, Munthu wina anatsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Yeriko; ndipo anagwa m'manja a achifwamba amene anamvula zovala, namkwapula, nachoka atamsiya wofuna kufa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Yesu adati, “Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Pa njira achifwamba adamgwira. Adamuvula zovala, nammenya, nkumusiya ali thasa, ali pafupi kufa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu pomuyankha anati, “Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Pa njira anavulazidwa ndi achifwamba. Anamuvula zovala zake, namumenya ndi kuthawa, namusiya ali pafupi kufa. |
Chifukwa chake, taona, masiku alinkudza, ati Yehova, amene ndidzaweruza mafano ake; ndipo padziko lake lonse olasidwa adzabuula.
Amati kwa amao, Tirigu ndi vinyo ali kuti? Pokomoka iwo ngati olasidwa m'makwalala a mzindawu, potsanulidwa miyoyo yao pa zifuwa za amao.
Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, ndi kuika lupanga langa m'dzanja lake; koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuula pamaso pake mabuulo a munthu wopyozedwa.
Ndipo kudangotero kuti wansembe wina anatsika njirayo, ndipo pakumuona iye anapita mbali ina.
Ndipo anadzitengera khumi ndi awiriwo, nati kwa iwo, Taonani, tikwera kunka ku Yerusalemu, ndipo zidzakwaniritsidwa kwa Mwana wa Munthu zonse zolembedwa ndi aneneri.