Ndipo pamene Iye anatuluka kutsata njira, anamthamangira munthu, namgwadira Iye, namfunsa, Mphunzitsi wabwino, ndidzachita chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?
Luka 10:25 - Buku Lopatulika Ndipo taonani, wachilamulo wina anaimirira namuyesa Iye, nanena, Mphunzitsi, ndidzalowa moyo wosatha ndi kuchita chiyani? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo taonani, wachilamulo wina anaimirira namuyesa Iye, nanena, Mphunzitsi, ndidzalowa moyo wosatha ndi kuchita chiyani? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Katswiri wina wa Malamulo adaimirira kuti ayese Yesu. Adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi ina katswiri wa malamulo anayimirira kuti ayese Yesu. Iye anati, “Aphunzitsi, ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?” |
Ndipo pamene Iye anatuluka kutsata njira, anamthamangira munthu, namgwadira Iye, namfunsa, Mphunzitsi wabwino, ndidzachita chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?
Ndipo anadza mmodzi wa alembi, namva iwo alikufunsana pamodzi, ndipo pakudziwa kuti anawayankha bwino, anamfunsa Iye, Lamulo la m'tsogolo la onse ndi liti?
Pakuti ndinena ndi inu kuti aneneri ndi mafumu ambiri anafuna kuona zimene inu muziona, koma sanazione; ndi kumva zimene mukumva, koma sanazimve.
Ndipo mkulu wina anamfunsa Iye, nanena, Mphunzitsi wabwino, ndizichita chiyani, kuti ndilowe moyo wosatha?
Koma Afarisi ndi achilamulo anakaniza uphungu wa Mulungu kwa iwo okha, popeza sanabatizidwe ndi iye.
Koma ichi ananena kuti amuyese Iye, kuti akhale nacho chomneneza Iye. Koma Yesu, m'mene adawerama pansi analemba pansi ndi chala chake.
Pakuti ngati kulowa nyumba kuchokera kulamulo, sikuchokeranso kulonjezano; koma kumeneku Mulungu anampatsa Abrahamu kwaufulu mwa lonjezano.