Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.
Luka 10:17 - Buku Lopatulika Ndipo makumi asanu ndi awiri aja anabwera mokondwera, nanena, Ambuye, zingakhale ziwanda zinatigonjera ife m'dzina lanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo makumi asanu ndi awiri aja anabwera mokondwera, nanena, Ambuye, zingakhale ziwanda zinatigonjera ife m'dzina lanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu 72 aja adabwerako ndi chimwemwe nati, “Ambuye, ngakhale mizimu yoipa yomwe imatigonjera tikamailamula m'dzina lanu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu 72 aja anabwerera ndi chimwemwe ndipo anati, “Ambuye, ngakhale ziwanda zinatigonjera ife mʼdzina lanu.” |
Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.
Ndipo zizindikiro izi zidzawatsata iwo akukhulupirira: m'dzina langa adzatulutsa ziwanda; adzalankhula ndi malankhulidwe atsopano;
Zitapita izi Ambuye anaika ena makumi asanu ndi awiri, nawatuma iwo awiriawiri pamaso pake kumudzi uliwonse, ndi malo ali onse kumene ati afikeko mwini.
Koma musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti maina anu alembedwa mu Mwamba.
ndipo chiritsani odwala ali momwemo nimunene nao, Ufumu wa Mulungu wayandikira kwa inu. Koma kumudzi uliwonse mukalowako,
Ndipo Iye anaitana pamodzi khumi ndi awiriwo nawapatsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse, ndi zakuchiritsa nthenda.
Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.