Luka 10:13 - Buku Lopatulika Tsoka iwe, Korazini! Tsoka iwe Betsaida! Chifukwa kuti zikadachitika mu Tiro ndi Sidoni zamphamvuzi zidachitika mwa inu, akadalapa kale lomwe ndi kukhala pansi ovala chiguduli ndi phulusa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsoka iwe, Korazini! Tsoka iwe Betsaida! Chifukwa kuti zikadachitika m'Tiro ndi Sidoni zamphamvuzi zidachitika mwa inu, akadalapa kale lomwe ndi kukhala pansi ovala chiguduli ndi phulusa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Uli ndi tsoka, iwe Korazini! Uli ndi tsoka, iwe Betsaida! Chifukwa zamphamvu zimene zidachitika mwa inu, achikhala zidaachitikira ku Tiro ndi ku Sidoni, bwenzi anthu ake atavala kale ziguduli nkudzithira phulusa, kuwonetsa kuti atembenukadi mtima. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ndiwe watsoka, iwe Korazini! Ndiwe watsoka, iwe Betisaida! Kukanakhala kuti zodabwitsa zimene zinachitika mwa inu zinachitika ku Turo ndi Sidoni, iwo akanatembenuka mtima kale lomwe, atavala ziguduli ndi kudzola phulusa. |
ndikakonzere iwo amene alira maliro mu Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.
Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chimodzi, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,
Ndipo ndinaika nkhope yanga kwa Ambuye Mulungu, kumfunsa Iye m'pemphero, ndi mapembedzero, ndi kusala, ndi ziguduli, ndi mapulusa.
Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Tiro, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anapereka anthu onse kwa Edomu, osakumbukira pangano lachibale;
m'maonekedwe onyenga a iwo onena mabodza, olochedwa m'chikumbu mtima mwao monga ndi chitsulo chamoto;
Ndipo ndidzalamulira mboni zanga ziwiri, ndipo zidzanenera masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri amphambu makumi asanu ndi limodzi, zovala chiguduli.