ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.
Luka 1:72 - Buku Lopatulika Kuchitira atate athu chifundo, ndi kukumbukira pangano lake lopatulika; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kuchitira atate athu chifundo, ndi kukumbukira pangano lake lopatulika; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Iye waŵachitiradi chifundo makolo athu akale, ndipo wakumbukira chipangano chake choyera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kuonetsa chifundo kwa makolo athu ndi kukumbukira pangano lake loyera, |
ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.
ndipo ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, ndipo ndidzapatsa mbeu zako maiko onsewa; m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa;
mbeu zako zidzakhala monga fumbi lapansi, ndipo udzabalalikira kumadzulo ndi kum'mawa ndi kumpoto ndi kumwera: mwa iwe ndi mu mbeu zako mabanja onse a dziko lapansi adzadalitsidwa.
Anakumbukira chifundo chake ndi chikhulupiriko chake kunyumba ya Israele; malekezero onse a dziko lapansi anaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Koma ndidzakumbukira Ine pangano langa ndi iwe m'masiku a ubwana wako, ndipo ndidzakhazikitsa pangano losatha nawe.
Ndipo popita Ine panali iwepo ndi kukupenya, taona nyengo yako ndiyo nyengo yakukondana; pamenepo ndinakufunda chofunda changa, ndi kuphimba umaliseche wako; inde ndinakulumbirira ndi kupangana nawe, ati Ambuye Yehova, ndipo unakhala wanga.
pamenepo ndidzakumbukira pangano langa ndi Yakobo; ndiponso pangano langa ndi Isaki, ndiponso pangano langa ndi Abrahamu ndidzakumbukira; ndipo ndidzakumbukira dzikoli.
Mudzapatsa kwa Yakobo choonadi, ndi kwa Abrahamu chifundo chimene munalumbirira makolo athu kuyambira masiku a kale lomwe.
Kunena za Uthenga Wabwino, iwo ali ngati adani, chifukwa cha inu; koma kunena za chisankhidwe, ali okondedwa, chifukwa cha makolo.
ndiwo Aisraele; ali nao umwana, ndi ulemerero, ndi mapangano, ndi kupatsa kwa malamulo, ndi kutumikira mu Kachisi wa Mulungu, ndi malonjezo;