ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.
Luka 1:70 - Buku Lopatulika Monga Iye analankhula ndi m'kamwa mwa aneneri ake oyera mtima, akale lomwe, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Monga Iye analankhula ndi m'kamwa mwa aneneri ake oyera mtima, akale lomwe, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Izi ndi zomwe Iye adaaneneratu kalekale kudzera mwa aneneri ake oyera mtima. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Monga mmene ananenera kudzera mwa aneneri oyera), |
ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.
ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.
Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.
Taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, ndidzamuukitsira Davide Mphukira wolungama, ndipo Iye adzakhala Mfumu, adzachita mwanzeru, nadzachita chiweruzo ndi chilungamo m'dziko lino.
Ndipo usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; usaope, iwe Israele; pakuti, taona, ndidzakupulumutsa iwe kutali, ndi mbeu zako kudziko la undende wao; ndipo Yakobo adzabwera, nadzakhala ndi mtendere, ndipo adzakhala chete, palibe amene adzamuopsa.
Davide mwini yekha anati mwa Mzimu Woyera, Ambuye anati kwa Ambuye wanga, Khala kudzanja langa lamanja, kufikira ndiwaika adani ako popondapo mapazi ako.
Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalimo.
Koma popeza sanavomerezane, anachoka atanena Paulo mau amodzi, kuti, Mzimu Woyera analankhula kokoma mwa Yesaya Mneneri kwa makolo anu,
Kwa iwo amene kudavumbulutsidwa, kuti sanadzitumikire iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.
pakuti kale lonse chinenero sichinadze ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.
kuti mukumbukire mau onenedwa kale ndi aneneri oyera, ndi lamulo la Ambuye ndi Mpulumutsi, mwa atumwi anu;
Ndipo ndinagwa pa mapazi ake kumlambira iye. Ndipo ananena ndi ine, Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako akukhala nao umboni wa Yesu; lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa chinenero.