natumiza ndi dzanja la Natani mneneriyo, namutcha dzina lake Wokondedwa ndi Yehova, chifukwa cha Yehova.
Luka 1:60 - Buku Lopatulika Ndipo amake anayankha, kuti, Iai; koma adzatchedwa Yohane. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo amake anayankha, kuti, Iai; koma adzatchedwa Yohane. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma mai wake adakana, adati, “Iyai, koma atchedwe Yohane.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero koma amayi ake anayankhula nati, “Ayi, atchulidwe kuti Yohane.” |
natumiza ndi dzanja la Natani mneneriyo, namutcha dzina lake Wokondedwa ndi Yehova, chifukwa cha Yehova.
Ndipo ndinanka kwa mneneri wamkazi; ndipo iye anatenga pakati nabala mwana wamwamuna. Ndipo Yehova anati kwa ine, Utche dzina lake, Kangazakufunkha Fulumirakusakaza.
Koma mngelo anati kwa iye, Usaope Zekariya, chifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane.
Ndipo iye anafunsa cholemberapo, nalemba, kuti, Dzina lake ndi Yohane. Ndipo anazizwa onse.