ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.
Luka 1:55 - Buku Lopatulika (Monga analankhula kwa makolo athu) kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake kunthawi yonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 (Monga analankhula kwa makolo athu) kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake kunthawi yonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Izi ndi zomwe adaalonjeza kuti adzaŵachitira makolo athu akale aja, Abrahamu ndi zidzukulu zake mpaka muyaya.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kwa Abrahamu ndi zidzukulu zake ku nthawi zonse monga ananena kwa makolo athu.” |
ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.
Ndipo Mulungu anati, Koma Sara mkazi wako adzakubalira iwe mwana wamwamuna; ndipo udzamutcha dzina lake Isaki; ndipo ndidzalimbikitsa naye pangano langa, kuti likhale pangano la nthawi zonse, la ku mbeu zake za pambuyo pake.
Ndipo ndidzalimbitsa pangano langa ndi Ine ndi iwe pa mbeu zako za pambuyo pako m'mibadwo yao, kuti likhale pangano la nthawi zonse, kuti ndikhale Mulungu wako ndi wa mbeu zako za pambuyo pako.
ndipo ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, ndipo ndidzapatsa mbeu zako maiko onsewa; m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa;
mbeu zako zidzakhala monga fumbi lapansi, ndipo udzabalalikira kumadzulo ndi kum'mawa ndi kumpoto ndi kumwera: mwa iwe ndi mu mbeu zako mabanja onse a dziko lapansi adzadalitsidwa.