Luka 1:47 - Buku Lopatulika ndipo mzimu wanga wakondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo mzimu wanga wakondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndipo mzimu wanga ukukondwera mwa Mulungu, Mpulumutsi wanga, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo mzimu wanga ukondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga, |
Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.
pakuti wakubadwirani inu lero, m'mzinda wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Khristu Ambuye.
Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu monga mwa chilamuliro cha Mulungu Mpulumutsi wathu, ndi cha Khristu Yesu, chiyembekezo chathu:
koma pa nyengo za Iye yekha anaonetsa mau ake muulalikiro, umene anandisungitsa ine, monga mwa lamulo la Mpulumutsi wathu Mulungu:
osatapa pa zao, komatu aonetsere chikhulupiriko chonse chabwino; kuti akakometsere chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu m'zinthu zonse.
akulindira chiyembekezo chodala, ndi maonekedwe a ulemerero wa Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu;
kwa Mulungu wayekha, Mpulumutsi wathu, mwa Yesu Khristu Ambuye wathu, kukhale ulemerero, ukulu, mphamvu, ndi ulamuliro zisanayambe nthawi, ndi tsopano, ndi kufikira nthawi zonse. Amen.