Ndipo Maria anati, Onani, mdzakazi wa Ambuye; kukhale kwa ine monga mwa mau anu. Ndipo mngelo anachoka kwa iye.
Luka 1:39 - Buku Lopatulika Ndipo Maria ananyamuka masiku amenewa, namuka ndi changu kudziko la mapiri kumzinda wa Yuda; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Maria ananyamuka masiku amenewa, namuka ndi changu kudziko la mapiri kumudzi wa Yuda; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Patapita masiku oŵerengeka, Maria adanyamuka napita mofulumira ku dera lamapiri, ku mudzi wina wa ku Yudeya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi imeneyo anakonzeka ndipo anapita mofulumira ku mudzi wa ku mapiri a dziko la Yudeya, |
Ndipo Maria anati, Onani, mdzakazi wa Ambuye; kukhale kwa ine monga mwa mau anu. Ndipo mngelo anachoka kwa iye.
Ndipo panagwa mantha pa iwo onse akukhala oyandikana nao; ndipo analankhulalankhula nkhani izi zonse m'dziko lonse la mapiri a Yudeya.
Motero Yoswa anakantha dziko lonse, la kumapiri, la kumwera, la kuchidikha, la kuzigwa, ndi mafumu ao onse; sanasiyepo ndi mmodzi yense; koma anaononga psiti zonse zampweya, monga Yehova Mulungu wa Israele adalamulira.
Ndipo anapatula Kedesi mu Galileya ku mapiri a Nafutali, ndi Sekemu ku mapiri a Efuremu, ndi mudzi wa Ariba ndiwo Hebroni ku mapiri a Yuda.