Luka 1:31 - Buku Lopatulika Ndipo taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamutcha dzina lake Yesu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamutcha dzina lake Yesu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mudzatenga pathupi, ndipo mudzabala mwana wamwamuna. Mudzamutcha dzina lake Yesu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Udzakhala woyembekezera ndipo udzabala mwana wamwamuna ndipo udzamupatse dzina loti Yesu. |
Chifukwa chake Ambuye mwini yekha adzakupatsani inu chizindikiro; taonani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, nadzamutcha dzina lake Imanuele.
Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo ao.
Onani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, ndipo adzamutcha dzina lake, Imanuele. Ndilo losandulika, Mulungu nafe.
Koma mngelo anati kwa iye, Usaope Zekariya, chifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane.
kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, dzina lake Yosefe, wa fuko la Davide; ndipo dzina lake la namwaliyo ndilo Maria.
Ndipo pamene panakwanira masiku asanu ndi atatu akumdula Iye, anamutcha dzina lake Yesu, limene anatchula mngeloyo asanalandiridwe Iye m'mimba.
koma pokwaniridwa nthawi, Mulungu anatuma Mwana wake, wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo,