Luka 1:29 - Buku Lopatulika Koma iye ananthunthumira ndi mau awa, nasinkhasinkha kulonjera uku nkutani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma iye ananthunthumira ndi mau awa, nasinkhasinkha kulonjera uku nkutani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Maria adadzidzimuka nawo kwambiri mau ameneŵa, nayamba kusinkhasinkha kuti kodi moni umenewu ndi wa mtundu wanji? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mariya anavutika kwambiri ndi mawu awa ndipo anadabwa ndi kulonjera kotere. |
Ndipo pakulowa mngelo anati kwa iye, Tikuoneni, wochitidwa chisomo, Ambuye ali ndi iwe.
Ndipo onse amene anazimva anazisunga m'mtima mwao, nanena, Nanga mwana uyu adzakhala wotani? Pakuti dzanja la Ambuye linakhala pamodzi ndi iye.
Ndipo anatsika nao pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo: ndipo amake anasunga zinthu izi zonse mumtima mwake.
Ndipo pokayikakayika Petro mwa yekha ndi kuti masomphenya adawaona akuti chiyani, taonani, amuna aja otumidwa ndi Kornelio, atafunsira nyumba ya Simoni, anaima pachipata,
Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuopa, anati, Nchiyani, Mbuye? Ndipo anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zachifundo zako zinakwera zikhala chikumbutso pamaso pa Mulungu.