Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Luka 1:26 - Buku Lopatulika

Ndipo mwezi wachisanu ndi chimodzi mngelo Gabriele anatumidwa ndi Mulungu kunka kumzinda wa ku Galileya dzina lake Nazarete,

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo mwezi wachisanu ndi chimodzi mngelo Gabriele anatumidwa ndi Mulungu kunka kumudzi wa ku Galileya dzina lake Nazarete,

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Elizabeti ali ndi pathupi pa miyezi isanu ndi umodzi, Mulungu adatuma mngelo Gabriele ku mudzi wina wa ku Galileya, dzina lake Nazarete.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mwezi wachisanu ndi chimodzi, Mulungu anatuma mngelo Gabrieli ku Nazareti, mudzi wa ku Galileya,

Onani mutuwo



Luka 1:26
8 Mawu Ofanana  

Ndipo ndinamva mau a munthu pakati pa magombe a Ulai, naitana, nati, Gabriele, zindikiritsa munthuyu masomphenyawo.


inde pakunena ine m'kupemphera, munthu uja Gabriele, amene ndidamuona m'masomphenya poyamba paja, anauluka mwaliwiro nandikhudza ngati nthawi yakupereka nsembe ya madzulo.


nadza nakhazikika m'mzinda dzina lake Nazarete kuti chikachitidwe chonenedwa ndi aneneri kuti, Adzatchedwa Mnazarayo.


Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Ine ndine Gabriele, woimirira pamaso pa Mulungu; ndipo ndinatumidwa kwa iwe kudzalankhula nawe, ndi kuuza iwe uthenga uwu wabwino.


Ndipo pamene iwo anatha zonse monga mwa chilamulo cha Ambuye, anabwera ku Galileya, kumzinda kwao, ku Nazarete.


Ndipo Yosefe yemwe anakwera kuchokera ku Galileya, kumzinda wa Nazarete, kunka ku Yudeya, kumzinda wa Davide, dzina lake Betelehemu, chifukwa iye anali wa banja ndi fuko lake la Davide;


Ena ananena, Uyu ndi Khristu. Koma ena ananena, Kodi Khristu adza kutuluka mu Galileya?